Ndandanda ya Mlungu wa August 9
MLUNGU WOYAMBIRA AUGUST 9
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Mafumu 21-22
Na. 1: 1 Mafumu 22:1-12
Na. 2: Kodi Munthu Akayamba Kuchita Nawo za M’dzikoli Chifukwa Chofuna Kudziimira Payekha, Amakhala Akulamuliridwa ndi Ndani? (rs tsa. 174 ndime 1-2)
Na. 3: Kodi Chitsanzo cha Eliya Chikutiphunzitsa Chiyani pa Nkhani ya Pemphero? (Yakobe 5:18)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 15: Kodi Mfundo Yoti Zamoyo Zinachita Kusanduka Imagwirizanadi ndi Sayansi? Nkhani yokambirana ndi omvera yochokera m’buku la Kukambitsirana, tsamba 99 ndime 1 mpaka tsamba 104 ndime 1. Pemphani omvera kuti afotokoze mmene anagwiritsira ntchito mfundo zimenezi polalikira kusukulu kapena malo ena.
Mph. 15: “Mayi Wathanzi Amaberekanso Mwana Wathanzi.” Nkhani ya mafunso ndi mayankho. Ikambidwe ndi mkulu woyenerera.