Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu September: Gawirani buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? October: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Anthu amene asonyeza chidwi agawireni kapepala kakuti, Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? ndipo yesetsani kuyambitsa phunziro la Baibulo. November: Gawirani buku lakuti, Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi? December: Gawirani buku lakuti, Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati mwapeza ana panyumba gawirani buku lakuti, Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso.
◼ Nkhani yapadera ya panyengo ya Chikumbutso cha 2011 idzaperekedwa mlungu woyambira April 25, 2011. Mutu wa nkhaniyi udzalengezedwa m’tsogolo. Mipingo imene idzakhale ndi woyang’anira dera kapena msonkhano wapadera mlungu umenewo adzakhala ndi nkhaniyi mlungu wotsatira. Mpingo uliwonse usadzakhale ndi nkhaniyi pasanafike pa April 25.