Ndandanda ya Mlungu wa October 4
MLUNGU WOYAMBIRA OCTOBER 4
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
lv mutu 13 ndime 1-4, ndi mabokosi pamasamba 148-149, 158-159
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Mbiri 1-4
Na. 1: 1 Mbiri 1:1-27
Na. 2: Zimene Kukhala Wodzetsa Mtendere Kumatanthauza (1 Pet. 3:10-12)
Na. 3: Kodi Mboni za Yehova Ndi Chipembedzo cha ku America, Nanga Amapeza Bwanji Ndalama Zoyendetsera Ntchito Yawo? (rs-CN tsa. 272 ndime 4–tsa. 273 ndime 3)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Chifukwa Chimene Timaperekera Lipoti la Utumiki Wathu Wakumunda. Nkhani yokambidwa ndi mlembi yochokera m’buku la Gulu, tsamba 88, ndime 1, mpaka tsamba 90, ndime 1.
Mph. 8: Zosowa za pampingo.
Mph. 12: Kodi Mungakonzekere Bwanji Kuthana ndi Mavuto a Kusukulu? Kukambirana ndi omvera. Pemphani omvera kuti afotokoze ena mwa mavuto amene Akhristu achinyamata amakumana nawo kusukulu. Fotokozani mmene makolo angagwiritsirire ntchito index, mabuku a Achinyamata Akufunsa ndiponso zofalitsa zina pa Kulambira kwa Pabanja kukonzekeretsa ana awo kuti athane ndi mayesero ndiponso kuti azifotokoza zimene amakhulupirira. (1 Pet. 3:15) Sankhani nkhani imodzi kapena ziwiri, ndipo fotokozani mfundo zothandiza zimene zikupezeka m’zofalitsa zathu. Pemphani omvera kuti afotokoze zimene anachita kuti athe kulalikira kusukulu.