Ndandanda ya Mlungu wa December 13
MLUNGU WOYAMBIRA DECEMBER 13
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
lv mutu 16 ndime 10-14, ndi bokosi patsamba 192-193
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 2 Mbiri 15-19
Na. 1: 2 Mbiri 15:8-19
Na. 2: **Ngati Wina Anena Kuti: “Akhristu Ayenera Kukhala Mboni za Yesu Osati za Yehova?” (rs tsa. 280 ndime 1)
Na. 3: Kodi Tingasonyeze Bwanji Ulemu Polambira Yehova?
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo. Limbikitsani onse kuti adzabweretse magazini ya Nsanja ya Olonda ya January 1, 2011, pobwera ku Msonkhano wa Utumiki wa mlungu wotsatira.
Mph. 15: Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya Chaka cha 2011. Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira sukulu. Pogwiritsa ntchito ndandanda ya 2011 tsindikani mfundo zimene mukuona kuti zingathandize kwambiri mpingo wanuwo. Fotokozani udindo wa mlangizi wothandiza. Limbikitsani onse kuchita khama kukwaniritsa mbali zawo, kutenga nawo mbali pa mfundo zazikulu, komanso kugwiritsa ntchito malangizo ochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki amene amaperekedwa mlungu uliwonse.
Mph. 15: “Kagwiritsireni Bwino Ntchito.” Nkhani ya mafunso ndi mayankho. Chitani chitsanzo chimodzi kapena ziwiri pogwiritsa ntchito malangizo amene ali mu nkhaniyo.