Ndandanda ya Mlungu wa July 4
MLUNGU WOYAMBIRA JULY 4
Nyimbo Na. 26 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 9 ndime 10-16 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Masalimo 60–68 (Mph. 10)
Na. 1: Salimo 62:1–63:5 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Tili Ndi Mbali Yotani pa Kukwaniritsidwa kwa Hagai 2:7? (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Ndani Amene Ali Olamulira mu Ufumuwo?—rs tsa. 375 ndime 3 mpaka 5 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Ngati Munthu Wanena Kuti: ‘Ndili Ndi Chipembedzo Changa.’ Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Kukambitsirana, tsamba 18 ndime 2 mpaka tsamba 19 ndime 4. Pemphani omvera kuti anene njira zina zomwe aona kuti n’zothandiza poyankha anthu otero. Chitani chitsanzo chimodzi kapena ziwiri zosonyeza mmene tingayankhire anthu pogwiritsa ntchito njira zimenezi.
Mph. 10: Kodi Tikuphunzirapo Chiyani? Nkhani yokambirana. Werengani Luka 9:57-62 ndi Luka 14:25-33. Kenako kambiranani mmene mavesiwa angatithandizire mu utumiki.
Mph. 10: Zosowa za pampingo.
Nyimbo Na. 50 ndi Pemphero