Ndandanda ya Mlungu wa July 11
MLUNGU WOYAMBIRA JULY 11
Nyimbo Na. 34 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 9 ndime 17-21 ndi bokosi patsamba 96 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Masalimo 69–73 (Mph. 10)
Na. 1: Salimo 72:1-20 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Ufumu wa Mulungu Udzakhudza Bwanji Maboma a Anthu?—rs tsa. 376 ndime 1-2 (Mph. 5)
Na. 3: Zimene Achinyamata Angaphunzire kwa Mfumu Hezekiya ndi Yosiya (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 30: “Masiku Atatu Otsitsimulidwa Mwauzimu.” Onani patsamba 3. Mafunso ndi mayankho. Kambiranani “Zofunika Kukumbukira pa Msonkhano Wachigawo.” Mukamakambirana ndime 5, funsani woyang’anira utumiki kuti afotokoze zimene zakonzedwa pa ntchito yogawira timapepala toitanira anthu kumsonkhano wachigawo.
Nyimbo Na. 30 ndi Pemphero