Ndandanda ya Mlungu wa July 25
MLUNGU WOYAMBIRA JULY 25
Nyimbo Na. 33 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 10 ndime 11-17 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Masalimo 79–86 (Mph. 10)
Na. 1: Salimo 84:1–85:7 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Ufumu wa Mulungu Udzagwirizanitsa Chilengedwe Chonse pa Kulambira Koyera—rs tsa. 377 ndime 1-2 (Mph. 5)
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Ziwanda Zonse Zimakhulupirira Kuti Kuli Mulungu?—Yak. 2:19 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo. Tchulani timabuku togawira m’mwezi wa August ndipo muchite chitsanzo chimodzi chosonyeza mmene mungagawirire timabukuto.
Mph. 10: Kodi Tikuphunzirapo Chiyani? Nkhani yokambirana. Werengani ndi kukambirana Yohane 4:3-24. Kambiranani mmene tingatsanzirire Yesu mu utumiki.
Mph. 20: “Magazini Athu Amakonzedwa Kuti Azifika Pamtima Anthu Onse.” Onani patsamba 7. Mafunso ndi mayankho. Mukamaliza kukambirana ndime yachiwiri, kambiranani kwa mphindi imodzi nkhani za m’magazini ya Galamukani! ya August. Kenako pemphani omvera kuti afotokoze mafunso ndi malemba amene angagwiritse ntchito pogawira magaziniwa. Ndiyeno muchite chitsanzo chosonyeza mmene mungagawirire magazini ya Galamukani! imeneyi. Mukamaliza kukambirana ndime yachitatu, chitaninso chimodzimodzi ndi Nsanja ya Olonda ya August 1.
Nyimbo Na. 55 ndi Pemphero