Ndandanda ya Mlungu wa August 1
MLUNGU WOYAMBIRA AUGUST 1
Nyimbo Na. 37 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 10 ndime 18-23 ndi bokosi patsamba 107 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Masalimo 87–91 (Mph. 10)
Na. 1: Salimo 89:26-52 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Zimene Zimachititsa Kuti Atumiki Okhulupirika a Yehova Azikhala Achimwemwe (Mph. 5)
Na. 3: Ufumu wa Mulungu Udzachotsa Nkhondo ndi Zachinyengo—rs tsa. 377 ndime 3–tsa. 378 ndime 2 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zilengezo. Pogwiritsa ntchito chitsanzo cha ulaliki chimene chili patsamba lino, chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungayambitsire phunziro la Baibulo Loweruka loyamba m’mwezi wa August. Limbikitsani onse kuti ayambitse maphunziro a Baibulo.
Mph. 15: Muzigwiritsa Ntchito Mafanizo Ophunzitsadi. Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 240-243. Pemphani omvera kuti afotokoze mafanizo achidule amene agwiritsapo ntchito mogwira mtima pokambirana ndi eninyumba kapena amene amaphunzira nawo Baibulo.
Mph. 10: Zosowa za pampingo.
Nyimbo Na. 54 ndi Pemphero