Ndandanda ya Mlungu wa August 8
MLUNGU WOYAMBIRA AUGUST 8
Nyimbo Na. 47 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 11, ndime 1-7 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Masalimo 92–101 (Mph. 10)
Na. 1: Salimo 94:1-23 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Ufumu wa Mulungu Udzapatsa Anthu Onse Chakudya Ndiponso Udzathetsa Matenda—rs tsa. 378 ndime 3-5 (Mph. 5)
Na. 3: Pewani Chinyengo Champhamvu Cha Chuma—Mat. 13:22 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo
Mph. 8: Muzisonyeza Chidwi kwa Eninyumba. Nkhani yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 186 mpaka 187. Chitani chitsanzo chachidule chosonyeza mmene mungagwiritsire ntchito mfundo imodzi kapena ziwiri za mu nkhaniyi.
Mph. 7: Zokumana Nazo Poyambitsa Maphunziro a Baibulo. Nkhani yokambirana, yokambidwa ndi woyang’anira utumiki. Yamikirani mpingo chifukwa chotsatira dongosolo loyambitsa maphunziro a Baibulo Loweruka loyambirira la mwezi. Pemphani omvera kunena zosangalatsa zimene akumana nazo. Chitani chitsanzo chimodzi kapena ziwiri cha zinthu zosangalatsa zimene zinachitika.
Mph. 15: “Kodi Ana Anu Akonzekera?” Mafunso ndi mayankho. Pemphani makolo ndi achinyamata kuti atchule mavuto enieni amene Akhristu amakumana nawo kusukulu. Mukamaliza kukambirana ndime 3, chitani chitsanzo chosonyeza bambo akukonzekeretsa mwana wake kukumana ndi mayesero. Bamboyo akhale ngati mphunzitsi ndipo mwanayo afotokozere mphunzitsiyo chifukwa chake sachita nawo masewera kapena zinthu zina za kusukuluko, zimene sizigwirizana ndi mfundo za m’Baibulo.
Nyimbo Na. 2 ndi Pemphero