Ndandanda ya Mlungu wa September 19
MLUNGU WOYAMBIRA SEPTEMBER 19
Nyimbo Na. 18 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 13 ndime 1-8 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Masalimo 135-141 (Mph. 10)
Na. 1: Salimo 137:1–138:8 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: N’chifukwa Chiyani Mawu a Paulo a pa Aroma 14:7-9 Ali Olimbikitsa? (Mph. 5)
Na. 3: Ufumu wa Mulungu Udzasandutsa Dziko Lapansili Kukhala Paradaiso—rs tsa. 380 ndime 6 mpaka tsa. 381 ndime 1 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Kodi Tinachita Zotani Chaka Chathachi? Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira utumiki. Fotokozani zimene mpingo wanu unachita mu utumiki m’chaka chautumiki chathachi, makamaka zinthu zabwino zimene unakwanitsa kuchita, ndipo uyamikireni mpingowo. Konzani zoti wofalitsa mmodzi kapena awiri adzafotokoze zinthu zolimbikitsa zimene anakumana nazo. Tchulani mfundo imodzi kapena ziwiri zimene mpingo wanu uyenera kukonza chaka talowachi, ndipo fotokozani zimene zingathandize mpingo wanu kuwongolera m’chaka chimenechi.
Mph. 10: Kodi Mungafotokoze? Nkhani yochokera m’buku la Gulu, tsamba 198, mafunso 12 ndi 13.
Mph. 10: “Yehova Akutiphunzitsa Kuti Tigwire Ntchitoyi.” Mafunso ndi mayankho.
Nyimbo Na. 47 ndi Pemphero