Zilengezo
◼ Mabuku ogawira m’mwezi wa September: Gawirani buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? October: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mukapeza anthu achidwi gawirani kapepala kakuti, Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? ndipo muyesetse kuyambitsa phunziro la Baibulo. November: Gawirani kabuku kakuti, Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani? December: Gawirani buku lakuti, Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati banjalo lili ndi ana mungagawire buku lakuti, Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso kapena Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo.
◼ Nkhani yapadera ya nyengo ya Chikumbutso cha 2012 idzakambidwa mlungu woyambira April 2. Mutu wa nkhaniyi udzalengezedwa m’tsogolo muno. Nkhaniyi isadzakambidwe mu mpingo uliwonse Chikumbutso chisanachitike.
◼ Ofalitsa ofuna kuchita upainiya wothandiza m’mwezi wa March 2012 adzakhala ndi mwayi wopereka maola 30 kapena 50 m’mwezi umenewo. Kuwonjezera pamenepa, ngati woyang’anira dera adzakhale akuchezera mpingo wanu m’mwezi wa March, onse amene adzakhale akuchita upainiya wothandiza kaya wa maola 30 kapena 50, akudziwitsidwa kuti adzakhale nawo pa msonkhano wonse umene woyang’anira dera amachititsa ndi apainiya okhazikika.
◼ M’mwezi wa September, oyang’anira dera adzayamba kukamba nkhani ya mutu wakuti, “Gwirizanani ndi Anthu Osangalala a Mulungu.”