Ndandanda ya Mlungu wa October 3
MLUNGU WOYAMBIRA OCTOBER 3
Nyimbo Na. 6 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 13 ndime 18-21 ndi bokosi patsamba 138 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Miyambo 1-6 (Mph. 10)
Na. 1: Miyambo 6:1-19 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Lemba la Aroma 8:26, 27 Limatitsimikizira Motani Kuti Mulungu Amatikonda? (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Ufumu wa Mulungu Udzayembekezera Kaye Kuti Anthu Onse Padziko Lapansi Atembenuke Usanabwere?—rs tsa. 381 ndime 5 mpaka tsa. 382 ndime 1 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Kodi Taphunzira Chiyani? Nkhani yokambirana. Werengani Luka 5:12, 13 ndi Luka 8:43-48. Kambiranani mmene nkhani zopezeka pa malembawa zingatithandizire mu utumiki.
Mph. 10: Zosowa za pampingo.
Mph. 10: Sonyezani Khalidwe Labwino mu Utumiki. (2 Akor. 6:3) Nkhani yokambirana. Gwiritsani ntchito mafunso otsatirawa pokambirana. (1) N’chifukwa chiyani tiyenera kusonyeza makhalidwe abwino tikamalalikira? (2) Kodi tingasonyeze bwanji makhalidwe abwino (a) gulu lathu likafika m’gawo limene timalalikira? (b) tikamayenda nyumba ndi nyumba? (c) tikafika pakhomo la mwininyumba? (d) mnzathu akamalalikira? (e) mwininyumba akamalankhula? (f) tikapeza mwininyumba ali wotanganidwa kapena ngati nyengo siili bwino? (g) ngati mwininyumba ndi wamwano?
Nyimbo Na. 16 ndi Pemphero