Ndandanda ya Mlungu wa October 10
MLUNGU WOYAMBIRA OCTOBER 10
Nyimbo Na. 26 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 14 ndime 1-9 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Miyambo 7-11 (Mph. 10)
Na. 1: Miyambo 8:1-21 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Ngati Wina Anena kuti: ‘Ufumu wa Mulungu Sudzabwera Ine Ndili Moyo’—rs tsa. 382 ndime 3 ndi 4 (Mph. 5)
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Malemba Amatichenjeza Kuti ‘Tisakhale Olungama Mopitirira Muyezo’?—Mlal. 7:16 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 15: Kodi Mwayesapo Kugwiritsa Ntchito? Nkhani yokambirana. Pokamba nkhaniyi, fotokozani mwachidule mfundo zopezeka mu nkhani yaposachedwapa mu Utumiki Wathu wa Ufumu yakuti: “Muzionetsetsa Kuti Mukulalikira Nawo Lamlungu,” (km 5/11) ndi yakuti, “Ulaliki wa Mumsewu Wopindulitsa,” (km 6/11). Pemphani omvera kuti afotokoze zimene ayesapo kuchita pogwiritsa ntchito mfundo za m’nkhanizi ndiponso zimene apindula.
Mph. 15: “Muzikambirana Ndi Mwininyumba.” Nkhani ya mafunso ndi mayankho. Mukamaliza kukambirana ndime 3, chitani chitsanzo chosonyeza wofalitsa akuyankha mwininyumba wotsutsa kapena amene wafunsa funso limene timafunsidwa kawirikawiri. Wofalitsayo ayankhe mwininyumba mokakamira kwambiri mfundo zake. Kenako wofalitsayo achitenso chitsanzo chosonyeza akuyankha funso lomwelo kapena kuyankha munthu wotsutsa mokambirana.
Nyimbo Na. 28 ndi Pemphero