Ndandanda ya Mlungu wa October 31
MLUNGU WOYAMBIRA OCTOBER 31
Nyimbo Na. 50 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 15 ndime 1-7 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Miyambo 22-26 (Mph. 10)
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu (Mph. 20)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zilengezo. “Kodi Likuoneka Bwanji?” Nkhani. Mukamaliza kukamba nkhaniyi, chitani chitsanzo pogwiritsa ntchito chitsanzo cha ulaliki chimene chili patsamba 8 kuti musonyeze mmene mungayambitsire phunziro pa Loweruka loyambirira m’mwezi wa November.
Mph. 15: Kufunika Kooneka Bwino mu Utumiki. Nkhani yokambirana yokambidwa ndi mkulu, yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 131 mpaka 134.
Mph. 10: Konzekerani Kugawira Magazini M’mwezi wa November. Nkhani yokambirana. Kwa mphindi imodzi kapena ziwiri, fotokozani nkhani za m’magaziniwo zimene zingakhale zogwira mtima kwa anthu a m’gawo lanu. Kenako, pogwiritsa ntchito nkhani zoyambirira mu Nsanja ya Olonda, pemphani omvera kuti afotokoze mafunso okopa chidwi amene angagwiritse ntchito ndiponso malemba amene angawerenge. Chitaninso chimodzimodzi ndi nkhani zoyambirira za mu Galamukani! ndipo ngati nthawi ilipo fotokozaninso nkhani imodzi. Chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungagawirire magazini iliyonse.
Nyimbo Na. 4 ndi Pemphero