Tizichita Maulendo Obwereza kwa Anthu Amene Anasonyeza Chidwi
1. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti anthu amene timawalalikira akule mwauzimu?
1 Mbewu zikabzalidwa zimafunika kuthiriridwa kuti zikule. Ndi mmenenso zimakhalira ndi mbewu za choonadi zimene zabzalidwa m’mitima ya anthu a m’gawo lathu. (1 Akor. 3:6) Choncho, ngati tikufuna kuti anthuwo akule mwauzimu, tiyenera kupanga maulendo obwereza kuti tizikathirira mbewu zophiphiritsira zimenezi pogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu.
2. Kodi tingachite chiyani kuti tikope chidwi mwininyumba kuti tidzakambirane nayenso pa ulendo wotsatira?
2 Muzifunsa mafunso: Mukamakonzekera zokanena mu ulaliki, muzikonzekeranso funso lochititsa chidwi loti mudzayankhe pa ulendo wobwereza. Muzifunsa funso limeneli kumapeto kwa ulendo woyamba ndipo muzikonza zoti mudzabwerenso. Abale ndi alongo ambiri amaona kuti kusankha nkhani inayake ya m’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani kumawathandiza kuti adzasonyeze munthuyo mmene amaphunzirira Baibulo.
3. Kodi mungalembe zinthu ziti zokhudza munthu amene mwamulalikira koyamba?
3 Muzilemba Zimene Mwakambirana: Mukangochoka pa nyumbayo, muzipeza nthawi yolemba zonse zimene mwakambirana ndi munthuyo. Muzilemba dzina la munthuyo ndi adiresi yake. Mungachite bwinonso kulemba tsiku, nthawi imene mwalankhula naye, zimene mwakambirana ndiponso mabuku ngati mwam’patsa buku lina lililonse. Kodi iye wanena kuti ali m’chipembedzo chinachake? Kodi ali ndi banja? Kodi wakuuzani zimene amakonda ndiponso zimene zimamudetsa nkhawa? Zimenezi zidzakuthandizani kuti mukamadzapitanso ulendo wina mudzakambirane naye nkhani zimene ali nazo chidwi. Muzilembanso tsiku ndi nthawi imene mwagwirizana kuti mudzabwerenso ndiponso funso limene mudzayankhe.
4. N’chifukwa chiyani sitiyenera kufooka pa nkhani yopitanso kwa anthu amene anasonyeza chidwi?
4 Musafooke: Satana adzachita zonse zimene angathe kuti ‘achotse mawu ofesedwa’ mumtima mwa munthu. (Maliko 4:14, 15) Choncho, musafooke ngati munthu amene anasonyeza chidwi sakupezekanso pakhomo lake. Mwina mungachite bwino kumulembera kakalata kapena kumusiyira uthenga. Mpainiya wina anayamba kuphunzira ndi mayi wina atangoima pakhomo la mayiyo. Kenako mayiyu sanapezekenso pa khomo, choncho mpainiyayo anangomulembera kalata. Koma tsiku lina mlongoyu anapeza mayiyu pakhomo ndipo mayiyo anayamikira kuchokera pansi pa mtima chifukwa chomuganizira kwambiri. Choncho, tikamathirira mbewu za choonadi, tingapeze chimwemwe tikamaona anthu akukula mwauzimu, kukhwima ndiponso ‘akubala zipatso wina 30, wina 60, ndipo wina 100.’—Maliko 4:20.