Zilengezo
◼ November: Gawirani kabuku kakuti, Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani? December: Gawirani buku lakuti, Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati pakhomopo pali ana, mungagawire buku lakuti, Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso kapena Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. January 2012: Gawirani buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Ndipo muyesetse kuyambitsa phunziro la Baibulo pa ulendo woyamba. Mungagawirenso magazini ena alionse akale amene sanawonongeke. February 2012 mudzagawire buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja.
◼ Mukamatumiza mwachindunji ku ofesi ya nthambi zopereka za ntchito ya padziko lonse, muzilemba kuti ziperekedwe ku “Watch Tower Society.” Adiresi ya ofesi ya nthambi ndi P.O. Box 30749, LILONGWE 3.