Ndandanda ya Mlungu wa December 5
MLUNGU WOYAMBIRA DECEMBER 5
Nyimbo Na. 53 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 16 ndime 15-20 ndi bokosi patsamba 171 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yesaya 1-5 (Mph. 10)
Na. 1: Yesaya 3:16-26; 4:1-6 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kukhala Maso Nthawi Zonse? (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Padziko Lapansi Padzatsala Anthu Pambuyo pa Chiwonongeko Cha Nthawi Ino?—rs tsa. 267 ndime 2 mpaka tsa. 268 ndime 1 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Mungayankhe Bwanji Wina Atakufunsani Chifukwa Chimene Simuchitira Nawo Khirisimasi? Nkhani yochokera m’buku la Kukambitsirana, tsamba 239 ndime 2 mpaka 242, ndime 3. Chitani chitsanzo chimodzi chachidule.
Mph. 10: Zosowa za pa mpingo.
Mph. 10: Muzikonzekera Ulaliki. Nkhani yokambirana pogwiritsa ntchito mafunso. (1) Kodi mumakonzekera bwanji, (a) ulaliki wa nyumba ndi nyumba? (b) ulendo wobwereza? (c) ulaliki wamwamwayi? (2) N’chifukwa chiyani tiyenera kukonzekera nthawi iliyonse imene tikukachititsa phunziro la Baibulo? (3) Kodi mumachita chiyani pothandiza wophunzira Baibulo kuti akonzekere zimene mudzaphunzire? (4) Kodi kukonzekera kumakuthandizani bwanji kuti muzisangalala ndi ulaliki? (5) N’chifukwa chiyani Yehova amasangalala tikamakonzekera ulaliki?
Nyimbo Na. 10 ndi Pemphero