Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira December 26, 2011.
1. Kodi tingapindule bwanji ndi malangizo opezeka pa Miyambo 27:21? [w06 9/15 tsa. 19, ndime 12]
2. Kodi ‘n’kusangalala’ kotani kumene kumasiya munthu ali wosakhutira? (Mlal. 2:1) [g 4/06 tsa. 6 ndime 1-2]
3. Ngakhale kuti anthu ambiri amanena kuti mawu a Solomo opezeka pa Mlaliki 3:1-9 amatsimikizira mfundo yoti Mulungu analemberatu zochitika pa moyo wathu, kodi zimene analemba pa Mlaliki 9:11 zimatithandiza bwanji kumvetsa mfundo yoti Mulungu sanalemberetu zinthu zimene zimatichitikira pa moyo? [w09 3/1 tsa. 4 ndime 4]
4. Kodi pamakhala ngozi yotani munthu akakhala “wolungama mopitirira muyezo”? (Mlal. 7:16) [w10 10/15 tsa. 9 ndime 8-9]
5. Kodi Nyimbo ya Solomo 2:7 ikusonyeza bwanji kuti amene akuganizira zolowa m’banja sayenera kuchita zinthu mopupuluma posankha womanga naye banja? [w06 11/15 tsa. 19 ndime 1; w80-E 4/15 tsa. 19 ndime 7]
6. Kodi mawu akuti ‘milomo yongokhalira kukha uchi wapachisa’ ndiponso ‘uchi ndi mkaka zili kuseri kwa lilime lake,’ la Msulami akutanthauza chiyani? (Nyimbo 4:11) [w06 11/15 tsa. 19 ndime 6]
7. Kodi mayina audindo akuti “Mlangizi Wodabwitsa,” “Mulungu Wamphamvu,” ndi “Atate Wosatha,” amatithandiza bwanji kuzindikira makhalidwe a Yesu ndiponso ulamuliro wake m’dziko lapansi latsopano? (Yes. 9:6) [w91 4/15 tsa. 5 ndime 7]
8. Kodi masiku ano “mtundu wopanduka” wa Isiraeli tingauyerekezere ndi ndani, ndipo ndani adzatumikira monga “ndodo” ya Yehova kuti auwononge? (Yes. 10:5, 6) [ip-1 tsa. 145 ndime 4, 5; tsa. 153 ndime 20]
9. N’chifukwa chiyani ulosi wa Yesaya wakuti m’Babulo “simudzakhalanso anthu” ndi wochititsa chidwi kwambiri, ndipo kodi kukwaniritsidwa kwake kukutitsimikizira chiyani masiku ano? (Yes. 13:19, 20) [g 11/07 tsa. 9 ndime 4-5]
10. Kodi Yesu analandira liti “makiyi a nyumba ya Davide,” ndipo wakhala akuwagwiritsa ntchito bwanji? (Yes. 22:22) [w09 1/15 tsa. 31 ndime 2]