Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu December: Gawirani buku lakuti, Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati pakhomopo pali ana, mungagawire buku lakuti, Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso kapena Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. January 2012: Gawirani buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Ndipo muyesetse kuyambitsa phunziro la Baibulo pa ulendo woyamba. Ngati mwininyumba ali nalo kale bukuli ndipo sakufuna phunziro la Baibulo, mungamupatse magazini ena alionse akale amene sanawonongeke kapena kabuku kalikonse kamene angakonde. February ndi March: Gawirani buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja ndi buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Mudzayesetse kuyambitsa phunziro la Baibulo pa ulendo woyamba.
◼ Chikumbutso cha chaka cha 2013 chidzachitika Lachiwiri, pa March 26.