Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu April ndi May: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mukapeza anthu achidwi, mungagawire kapepala kakuti, Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? ndipo muyesetse kuyambitsa phunziro la Baibulo. Mukamapanga maulendo obwereza kwa anthu amene anapezeka pa Chikumbutso kapena pamisonkhano ina, muziyesetsa kuyambitsa phunziro la Baibulo pogwiritsa ntchito buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. June: Gawirani buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Muyesetse kuyambitsa maphunziro a Baibulo pa ulendo woyamba. July: Mukamachita maulendo obwereza sonyezani mwininyumba buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Ngati mukuona kuti n’koyenera, mungamusonyeze kabuku kakuti Mverani Mulungu kapena kakuti Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha. Muyesetse kuyambitsa phunziro la Baibulo.