Ndandanda ya Mlungu wa May 21
MLUNGU WOYAMBIRA MAY 21
Nyimbo Na. 34 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 6 ndime 9-16 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yeremiya 44-48 (Mph. 10)
Na. 1: Yeremiya 46:18-28 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Mariya Anabadwa Ali Wangwiro?—rs tsa. 257 ndime 3 mpaka tsa. 258 ndime 1 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Tingatani Kuti Tizifesa ‘Motsatira Mzimu wa Mulungu’?—Agal. 6:8 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zilengezo. Tchulani mabuku ogawira m’mwezi wa June. Kenako muchite chitsanzo chimodzi chosonyeza mmene tingagawirire bukulo.
Mph. 15: Kodi Achinyamata, Mungachite Upainiya Wothandiza Mukatsekera Sukulu? Nkhani. Fotokozani mwachidule zimene zili m’buku la Gulu, patsamba 113 ndime yoyamba, pamene akufotokoza zimene munthu angachite kuti ayenerere kukhala mpainiya wothandiza. Kenako funsani wofalitsa mmodzi kapena awiri amene anachitapo upainiya wothandiza ali pa holide kusukulu. Limbikitsani achinyamata kuti adzachite upainiya wothandiza akatsekera kusukulu.
Mph. 10: “Muzigwiritsa Ntchito Mwaluso ‘Lupanga la Mzimu.’” Mafunso ndi mayankho.
Nyimbo Na. 41 ndi Pemphero