Ndandanda ya Mlungu wa August 6
MLUNGU WOYAMBIRA AUGUST 6
Nyimbo Na. 101 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 10 ndime 1-9 ndi bokosi patsamba 79 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Ezekieli 24–27 (Mph. 10)
Na. 1: Ezekieli 24:15-27 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Mulungu Ankalola Aisiraeli Kumenya Nkhondo pa Zifukwa Ziti?—rs tsa. 370 ndime 2 mpaka tsa. 371 ndime 3 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Lemba Ezekieli 18:20 Limatsutsana Ndi la Ekisodo 20:5? (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Kodi Mwakhonzekera Kulimbana Ndi Mayesero Kusukulu? Nkhani yokambirana. Pemphani omvera kuti afotokoze ena mwa mavuto amene Akhristu achinyamata amakumana nawo kusukulu. Fotokozani mmene makolo angagwiritsirire ntchito buku la Index, mabuku a Zimene Achinyamata Amafunsa ndiponso zofalitsa zina, pa kulambira kwa pabanja kuti akonzekeretse ana awo kuthana ndi mayesero ndiponso kuti azifotokoza zimene amakhulupirira. (1 Pet. 3:15) Sankhani nkhani imodzi kapena ziwiri, ndipo fotokozani mfundo zothandiza zimene zikupezeka m’zofalitsa zathu. Pemphani omvera kuti afotokoze zimene anachita kuti athe kulalikira kusukulu.
Mph. 10: Zosowa za pampingo.
Mph. 10: Zimene Munganene Pogawira Magazini M’mwezi wa August. Nkhani yokambirana. Kwa masekondi 30 mpaka 60 fotokozani mmene magaziniwo angakhalire ogwira mtima kwa anthu a m’gawo lanu. Kenako, pogwiritsa ntchito nkhani zoyambirira za mu Nsanja ya Olonda, pemphani omvera kuti afotokoze mafunso amene angakope chidwi cha anthu ndiponso malemba amene angawerenge. Chitaninso chimodzimodzi ndi nkhani zoyambirira za mu Galamukani! Ngati nthawi ilipo chitaninso chimodzimodzi ndi nkhani zina za m’magaziniwa. Chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungagawirire magazini iliyonse.
Nyimbo Na. 97 ndi Pemphero