Ndandanda ya Mlungu wa December 10
MLUNGU WOYAMBIRA DECEMBER 10
Nyimbo Na. 30 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 16 ndime 1-7, ndi bokosi patsamba 128 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Zefaniya 1-3–Hagai 1-2 (Mph. 10)
Na. 1: Hagai 1:1-13 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Anthu Anayamba Bwanji Kutsatira Nzeru za Anthu?—rs tsa. 137 ndime 1-3 (Mph. 5)
Na. 3: Kukhala Ndi Maganizo a Khristu Kumatithandiza Kudziwa Kwambiri Yehova—Mat. 11:27 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 15: Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya 2013. Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira sukulu. Pogwiritsa ntchito ndandanda ya Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya 2013, kambiranani mfundo zimene mukuona kuti zingathandize kwambiri mpingo wanu. Limbikitsani onse kuti azikonzekera mwakhama nkhani zawo, azipereka ndemanga pa mfundo zazikulu, komanso azigwiritsa ntchito malangizo ochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki amene amaperekedwa mlungu uliwonse.
Mph. 15: “Khalani Mwamtendere ndi Anthu Onse.” Mafunso ndi mayankho. Chitani chitsanzo chosonyeza wofalitsa akuyankha mosayenera mwininyumba wolusa. Kenako muchitenso chitsanzo china chosonyeza wofalitsayo akuyankha moyenera mwininyumba wolusa.
Nyimbo Na. 39 ndi Pemphero