Ndandanda ya Mlungu wa February 4
MLUNGU WOYAMBIRA FEBRUARY 4
Nyimbo Na. 92 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 18 ndime 12-18 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Mateyu 22-25 (Mph. 10)
Na. 1: Mateyu 23:25-39 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: N’chifukwa Chiyani Akhristu Ayenera Kuchita Chidwi ndi Maulosi a M’Baibulo?—rs tsa. 390 ndime 3-7 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Ndi Anthu ati Otchulidwa M’Baibulo Omwe Anatsatira Malangizo a pa Miyambo 3:5? (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zimene Munganene Pogawira Magazini mu February. Nkhani yokambirana. Kwa masekondi 30 mpaka 60, fotokozani chifukwa chake magaziniwo angakhale othandiza m’gawo lanu. Kenako, pogwiritsa ntchito nkhani zoyambirira za mu Nsanja ya Olonda, pemphani omvera kuti anene funso lochititsa chidwi ndiponso lemba limene angawerenge pogawira magaziniwo. Chitaninso chimodzimodzi ndi nkhani zoyambirira m’magazini ya Galamukani! Ngati nthawi ilipo mungachitenso zimenezi ndi nkhani ina imodzi m’magazini ya Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! Chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungagawirire magazini iliyonse.
Mph. 10: Ngati Wina Atanena Kuti ‘Sindimakhulupirira Mulungu’ Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Kukambitsirana tsamba 311, ndime 5 mpaka tsamba 312, ndime 2. Chitani chitsanzo chimodzi chachidule.
Mph. 10: Zosowa za pampingo.
Nyimbo Na. 95 ndi Pemphero