Ndandanda ya Mlungu wa March 3
MLUNGU WOYAMBIRA MARCH 3
Nyimbo Na. 85 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 8 ndime 8-13 ndi bokosi patsamba 98 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Genesis 36-39 (Mph. 10)
Na. 1: Genesis 37:1-17 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Chifukwa Chimene Anthu Oukitsidwa Sadzalangidwira Ntchito Zawo Zakale—rs tsa. 111 ndime 4 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Akhristu Angaphunzire Chiyani Kwa Abigayeli?—1 Sam. 25:14-35 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zimene Munganene Pogawira Magazini a March. Nkhani yokambirana. Yambani ndi kuchita chitsanzo cha mmene tingagawirire magaziniwo pogwiritsa ntchito zitsanzo za ulaliki zimene zili patsamba lino. Kenako kambiranani chitsanzo cha ulaliki chilichonse kuyambira poyambirira mpaka pamapeto. Pomaliza, funsani omvera kuti afotokoze mmene angagawirire magazini limodzi ndi kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso kumapeto kwa mlungu, pa milungu iwiri yomalizira m’mweziwo.
Mph. 10: Zosowa za pampingo.
Mph. 10: Kodi Tinachita Zotani? Nkhani yokambirana. Pemphani omvera kuti afotokoze mmene anapindulira pogwiritsa ntchito malangizo a m’nkhani yakuti, “Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Lembani Zokhudza Anthu Achidwi.” Kenako apempheni kuti anene zinthu zosangalatsa zimene anakumana nazo.
Nyimbo Na. 95 ndi Pemphero