Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu June: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? kapena gawirani timapepala totsatirati: Kodi Baibulo Mumalikhulupirira?, Kodi Mukuganiza Kuti Zinthu Zidzakhala Bwanji M’tsogolo?, Kodi N’chiyani Chingathandize Kuti Banja Likhale Losangalala?, Kodi Dziko Lapansili Lili M’manja mwa Ndani? kapena kakuti, Kodi Mavuto Amene Tikukumana Nawowa Adzathadi? July: Gawirani timabuku totsatirati: Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu, Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha, Kodi Mulungu Amatisamaliradi? ndi kakuti, Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu! August: Tidzagwira ntchito yapadera yogawira kapepala katsopano kodziwitsa anthu za webusaiti yathu ya jw.org/ny. September: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!
◼ Kuyambira kumapeto kwa chaka chautumiki cha 2014, Sukulu ya Utumiki Waupainiya izidzachitika kwa masiku 6, kuchokera Lolemba mpaka Loweruka.