Ndandanda ya Mlungu wa July 14
MLUNGU WOYAMBIRA JULY 14
Nyimbo Na. 47 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 13 ndime 20-26 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Levitiko 21-24 (Mph. 10)
Na. 1: Levitiko 23:1-14 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Zoti Anthu Onse Adzapulumuka Si za M’Malemba—rs tsa. 94 ndime 3 (Mph. 5)
Na. 3: Muzigwiritsa Ntchito Mwanzeru Nthawi Yovomerezeka Imene Muli Nayo Potumikira Mulungu—2 Akor. 6:2; Aheb. 3:7-8 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Konzekerani Kudzagwira Nawo Ntchito Yapadera mu August. Gawani kapepala katsopano kakuti, Mayankho a Mafunso Ofunika Kwambiri Okhudza Moyo kwa onse amene alibe kapepalaka. Pogwiritsa ntchito chitsanzo cha ulaliki chomwe chili patsamba 8, chitani zitsanzo ziwiri zosonyeza mmene tingagawirire kapepalaka. Chitsanzo choyamba chisonyeze mmene tingagawirire kapepalaka kwa anthu onse. Chachiwiri chisonyeze zimene tinganene ngati munthu amene tamugawira kapepalaka wasonyeza kuti akufuna kudziwa zambiri. Limbikitsani onse kuti adzagwire nawo ntchito yapadera imeneyi.
Mph. 5: Muzigwiritsa Ntchito Kabuku Kakuti, Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku. Nkhani yokambirana. Pemphani omvera kuti anene nthawi imene amapanga lemba la tsiku komanso mmene apindulira.
Mph. 15: “Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Mmene Tingayambire Ulaliki Wamwamwayi.” Nkhani yokambirana. Chitani chitsanzo chimodzi.
Nyimbo Na. 107 ndi Pemphero