Ndandanda ya Mlungu wa July 28
MLUNGU WOYAMBIRA JULY 28
Nyimbo Na. 21 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 14 ndime 8-13 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Numeri 1-3 (Mph. 10)
Na. 1: Numeri 3:21-38 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: ‘Anthu a Mitundu Yonse’ Adzapulumuka—rs tsa. 95 ndime 2 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Nkhani Zokhudza Kuimbidwa Mlandu Zinkasamalidwa Bwanji Nthawi Imene Malamulo a Aheberi Ndiponso a Aroma Ankagwira Ntchito?—Lev. 5:1; 24:11-14; Deut. 19:16-19; Mac. 23: 30, 35 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Kodi Mwakonzekera Bwanji Mavuto a ku Sukulu? Nkhani yokambirana. Pemphani omvera kuti anene mavuto amene Akhristu achinyamata amakumana nawo kusukulu. Fotokozani mmene makolo angagwiritsire ntchito webusaiti yathu ndi mabuku athu kuti athandize ana awo kukonzekera mayesero amene angakumane nawo kusukulu. (1 Pet. 3:15) Sankhani vuto limodzi kapena awiri, ndipo fotokozani mfundo zothandiza zimene zili m’mabuku athu. Pemphani omvera kuti afotokoze zimene ankachita kuti azitha kulalikira kusukulu.
Mph. 10: Funsani Mlembi. Kodi ntchito yanu ndi yotani? Kodi oyang’anira timagulu ndiponso ofalitsa angathandize bwanji kuti muthe kulemba lipoti la utumiki lolondola komanso pa nthawi yake? Kodi lipoti lolondola limathandiza bwanji akulu, oyang’anira madera komanso ofesi ya nthambi kudziwa ngati pakufunika kulimbikitsa mpingo pa mbali inayake?
Mph. 10: “Tengerani Chitsanzo kwa Aneneri—Zefaniya.” Onani tsamba 6. Mafunso ndi mayankho.
Nyimbo Na. 70 ndi Pemphero