Ndandanda ya Mlungu wa September 8
MLUNGU WOYAMBIRA SEPTEMBER 8
Nyimbo Na. 132 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 1 ndime 1-9 ndi bokosi patsamba 3 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Numeri 22-25 (Mph. 10)
Na. 1: Numeri 22:36-41 ndi 23:1-10 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Satana Si Maganizo Oipa Chabe Amene Anthu Angakhale Nawo—rs tsa. 353 ndime 2-4 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Adamu Analengedwa M’chifanizo cha Mulungu M’njira Iti?—Gen. 1:26 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 15: Muzisonyeza Makhalidwe Abwino Mukamalalikira. (2 Akor. 6:3) Nkhani yokambirana pogwiritsa ntchito mafunso awa: (1) N’chifukwa chiyani tiyenera kusonyeza makhalidwe abwino tikamalalikira? (2) Kodi tingasonyeze bwanji makhalidwe abwino (a) kagulu kathu kakafika m’gawo lomwe tikulalikira? (b) tikamachoka panyumba ina kupita kunyumba ina kapena tikamayendetsa galimoto kudera lakumudzi? (c) tikafika panyumba ya munthu? (d) munthu amene tayenda naye akamalankhula ndi munthu yemwe akumulalikira? (e) munthu amene tikumulalikira akamalankhula? (f) tikapeza munthu ali wotanganidwa kapena ngati nyengo sili bwino? (g) munthu amene tamupeza akakhala wamwano?
Mph. 15: “Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Muzisiya Funso Loti Mudzakambirane pa Ulendo Wotsatira.” Nkhani yokambirana. Chitani chitsanzo chosonyeza wofalitsa akulankhula yekha pokonzekera ulaliki. Akukonzekeranso funso lomwe akafunse munthu amene walandira magazini, n’cholinga choti adzalikambirane pa ulendo wotsatira.
Nyimbo Na. 68 ndi Pemphero