Ndandanda ya Mlungu wa October 6
MLUNGU WOYAMBIRA OCTOBER 6
Nyimbo Na. 22 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 2 ndime 12-20 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Deuteronomo 1-3 (Mph. 10)
Na. 1: Deuteronomo 2:16-30 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Tatsala Pang’ono Kupeza Mpumulo ku Zinthu Zoipa Zimene Satana Amatilimbikitsa Kuchita—rs tsa. 356 ndime 3–tsa. 357 ndime 2 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Kuti Kugonana Konse Ndi Tchimo?—rs tsa. 179 ndime 1–tsa. 180 ndime 3 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zimene Munganene Pogawira Magazini a October. Nkhani yokambirana. Pogwiritsa ntchito zitsanzo za ulaliki zimene zili patsamba lino, yambani ndi kuchita chitsanzo cha mmene tingagawirire magaziniwo. Kenako kambiranani zitsanzozi, kuyambira poyamba mpaka pamapeto.
Mph. 10: Zosowa za pampingo.
Mph. 10: Kodi Tinachita Zotani? Nkhani yokambirana. Pemphani omvera kuti afotokoze mmene anapindulira pogwiritsa ntchito malangizo a m’nkhani yakuti, “Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Muzisiya Funso Loti Mudzakambirane pa Ulendo Wotsatira.” Kenako apempheni kuti anene zinthu zosangalatsa zimene anakumana nazo.
Nyimbo Na. 83 ndi Pemphero