Ndandanda ya Mlungu wa October 20
MLUNGU WOYAMBIRA OCTOBER 20
Nyimbo Na. 15 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 3 ndime 1-10 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Deuteronomo 7-10 (Mph. 10)
Na. 1: Deuteronomo 9:15-29 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Chifukwa Chake Zinali Zotheka Kuti Munthu Wangwiro Achimwe—rs tsa. 358 ndime 1-4 (Mph. 5)
Na. 3: Tisamakayikire Zimene Yehova Wasankha—Aroma 11:33; 1 Yoh. 4:8 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 15: “Mmene Tingafotokozere Zimene Timakhulupirira Zokhudza Chaka cha 1914.” Nkhani yokambirana. Funsani omvera kuti ayankhe mafunso omwe ali ndi timadonthowo.
Mph. 15: Nkhani Zomwe Zingatithandize Kufotokoza Zomwe Timakhulupirira Zokhudza 1914. Yambani ndi kuchita chitsanzo cha mphindi 7 pogwiritsa ntchito tchati chomwe chili mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 2014, patsamba 11. Chitsanzocho chisonyeze wofalitsa akufotokozera munthu amene amaphunzira naye Baibulo mmene ulosi wopezeka pa Danieli chaputala 4 ukugwirizanirana ndi Ufumu wa Mulungu. Pemphani omvera kuti afotokoze zomwe wofalitsayo anachita zimene zathandiza wophunzira Baibuloyo. Pomaliza werengani Chivumbulutso 12:10, 12 ndipo pemphani omvera kuti afotokoze chifukwa chake kudziwa kuti Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira mu 1914 kumatithandiza kuti tizilalikira modzipereka.
Nyimbo Na. 133 ndi Pemphero