Ndandanda ya Mlungu wa December 8
MLUNGU WOYAMBIRA DECEMBER 8
Nyimbo Na. 15 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 5 ndime 9-17 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yoswa 1-5 (Mph. 10)
Na. 1: Yoswa 1:1-18 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Mzimu Woyera N’chiyani?—rs tsa. 319 ndime 2–tsa. 320 ndime 1 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Munthu Angachite Bwanji Chigololo Chauzimu?—lv tsa. 51-53 ndime 3-6 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: Tizipereka zinthu “zabwino” zochokera m’chuma chomwe tinapatsidwa.—Mat. 12:35a.
Mph. 10: Zinthu “Zabwino” Zimene Tiphunzire Mwezi Uno. Nkhani. Tchulani mutu wa mwezi uno. (Mat. 12:35a) Munthu amene anatiphunzitsa choonadi tingati anatipatsa chuma chauzimu. (Onani Nsanja ya Olonda ya April 1, 2002, tsamba 16, ndime 5 mpaka 7.) Nafenso tiyenera kuuza ena zinthu “zabwino” zomwe taphunzira. (Agal. 6:6) Tchulani zinthu “zabwino” zomwe tiphunzire mu Msonkhano wa Utumiki mwezi uno. Tiphunzira zimene tingachite kuti tiziphunzitsa mwaluso. Tiphunziranso nyimbo zatsopano.
Mph. 20: “Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Tizisonyeza Anthu Mmene Timaphunzirira Baibulo Pogwiritsa Ntchito Buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani.” Nkhani yokambirana. Pemphani wofalitsa waluso kapena mpainiya kuti achite chitsanzo chosonyeza mmene tingachititsire phunziro la Baibulo pogwiritsa ntchito buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani.
Nyimbo Na. 96 ndi Pemphero