Ndandanda ya Mlungu wa December 22
MLUNGU WOYAMBIRA DECEMBER 22
Nyimbo Na. 132 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 6 ndime 1-8 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yoswa 9-11 (Mph. 10)
Na. 1: Yoswa 9:16-27 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Palibe Mbali ya Munthu Imene Imakhalabe ndi Moyo Munthu Akafa—rs tsa. 321 ndime 6–tsa. 322 ndime 3 (Mph. 5)
Na. 3: Chifukwa Chake Tiyenera Kukhala pa Ubwenzi Wabwino ndi Yehova Ndiponso Anthu Amene Amamukonda—lv tsa. 26-27 ndime 4-7 ndi bokosi patsamba 29 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: Tizipereka zinthu “zabwino” zochokera m’chuma chomwe tinapatsidwa.—Mat. 12:35a.
Mph. 5: Zofunika pampingo.
Mph. 25: “Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya 2015 Itithandiza Kuti Tiziphunzitsa Mwaluso.” Nkhani yokambirana yokambidwa ndi woyang’anira sukulu. Woyang’anira sukulu angasankhe kuti ndime zina ziwerengedwe musanazikambirane. Fotokozani chimene chasintha pa nkhani Na. 1, nthawi ya mfundo zazikulu za Baibulo komanso malangizo omwe woyang’anira sukulu azipereka. Werengani ndime 7 ndipo mukamaliza kuikambirana chitani chitsanzo chosonyeza mkulu akuchita kulambira kwa pabanja ndi mkazi komanso mwana wake pogwiritsa ntchito nkhani yomwe ili patsamba 14 m’kabuku kakuti, Kodi M’Baibulo Muli Nkhani Zotani? Limbikitsani onse kuti ayesetse kupindula mokwanira ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Alimbikitseninso kuti azigwiritsa ntchito bwino buku la Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu.
Nyimbo Na. 117 ndi Pemphero