Ndandanda ya Mlungu wa December 29
MLUNGU WOYAMBIRA DECEMBER 29
Nyimbo Na. 35 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 6 ndime 9-15 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yoswa 12-15 (Mph. 10)
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu (Mph. 20)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: Tizipereka zinthu “zabwino” zochokera m’chuma chomwe tinapatsidwa.—Mat. 12:35a.
Mph. 20: Muzichitira Ena “Zabwino” Pophunzitsa Mogwira Mtima Ana Anu Komanso Anthu Amene Mumaphunzira Nawo Baibulo. (Mat. 12:35a) Nkhani yokambirana. Gwiritsani ntchito malemba awa posonyeza zomwe tiyenera kuyembekezera kwa ana komanso anthu omwe timaphunzira nawo Baibulo: 1 Akorinto 13:11 ndi 1 Petulo 2:2, 3. Fotokozani kuti ‘kulawa mkaka wosasukuluka umene uli m’mawu a Mulungu’ kukutanthauza chiyani. Fotokozaninso mmene tingathandizire anthu omwe timaphunzira nawo Baibulo komanso ana athu kuchita zimenezi. Tchulani mfundo yaikulu ya lemba la Maliko 4:28. (Onani Nsanja ya Olonda ya December 15, 2014, tsamba 12 ndime 6 mpaka 8.) Funsani wofalitsa waluso kapena kholo kuti afotokoze mmene anathandizira wophunzira Baibulo kapena mwana wake kuti apite patsogolo mwauzimu.—Aef. 4:13-15; Onani Bokosi la Mafunso mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa May 2014.
Mph. 10: “Tizichitira Ena ‘Zabwino’ Pokhala Ochereza (Mat. 12:35a).” Nkhani yokambirana. Fotokozani mmene anthu ena apindulira pochereza ena kapena zosangalatsa zomwe zinachitika pamene ankachereza. Pemphani omvera kuti afotokoze mmene tingasonyezere kuti ndife ochereza anthu, makamaka amene ali mu utumiki wa nthawi zonse. Fotokozaninso zimene mpingo ungachite pa nkhani yochereza m’bale amene wabwera kudzakamba nkhani ku mpingo wanu.
Nyimbo Na. 124 ndi Pemphero