Ndandanda ya Mlungu wa February 16
MLUNGU WOYAMBIRA FEBRUARY 16
Nyimbo Na. 111 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 8 ndime 17-24 ndi bokosi patsamba 86 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Oweruza 15-18 (Mph. 8)
Na. 1: Oweruza 16:13-24 (Osapitirira mph. 3)
Na. 2: Kodi Yehova Amamva Bwanji Tikamavutika?—bt tsa. 60-61 ndime 5-7 (Mph. 5)
Na. 3: Apolo Anali Wodzichepetsa, Wophunzitsa Mwaluso Komanso Wakhama—Mac. 18:24-28 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: Khalani “Odzipereka pa Ntchito Zabwino”—Tito 2:14.
Mph. 15: Muzikonzekera Kulalikira Uthenga Wabwino Modzipereka. Nkhani yokambirana. N’chifukwa chiyani tiyenera kupemphera tisanalowe mu utumiki? (Sal. 143:10; Mac. 4:31) Kuwonjezera pa pemphero, kodi chinanso chofunika n’chiyani? (Ezara 7:10) Tikapemphera komanso kukonzekeretsa mtima wathu, ndi zinthu zinanso ziti zomwe tiyenera kuchita? Kodi kukonzekera bwino kumatithandiza bwanji? (Onani Nsanja ya Olonda ya July 15, 2008, tsamba 10, ndime 9.) Kodi tingakonzekere bwanji utumiki? Chitani chitsanzo chosonyeza wofalitsa akukonzekera kulowa mu utumiki. Wofalitsayo akuonanso nkhani zomwe zili m’kapepala, m’kabuku kapena m’magazini omwe akufuna kukagwiritsa ntchito. Kenako akulongedza mabukuwo m’chikwama ndipo akuonetsetsa kuti ali ndi zonse zofunika. Pomaliza limbikitsani onse kuti azikonzekera asanalowe mu utumiki.—2 Tim. 3:17.
Mph. 15: “Kodi Mutsanzira Kudzipereka kwa Yehova ndi Yesu pa Nyengo ya Chikumbutso Ikubwerayi?” Mafunso ndi mayankho. Gawirani aliyense kapepala kamodzi koitanira anthu ku Chikumbutso ndipo kambiranani zimene zili m’kapepalako. Chitani chitsanzo chachidule pogwiritsa ntchito chitsanzo cha ulaliki chomwe chili patsamba 4.
Nyimbo Na. 30 ndi Pemphero