Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu March ndi April: Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! May ndi June: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? kapena kapepala kakuti, Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? Mungathenso kugwiritsa ntchito timapepala tatsopano poyamba kukambirana ndi anthu oyandikana nawo nyumba, anzanu a kusukulu, a kuntchito, polalikira kunyumba ndi nyumba kapena poyambitsa phunziro.
◼ Chikumbutso cha chaka chino chidzachitika Lachisanu pa 3 April, 2015. Ngati mpingo wanu umachita misonkhano Lachisanu, mungakonze zoti misonkhanoyi idzachitike tsiku lina mlungu womwewo. Koma ngati n’zosatheka kuchita misonkhanoyi mkati mwa mlunguwo, wogwirizanitsa ntchito za akulu angasankhe nkhani za mu Msonkhano wa Utumiki zimene akuona kuti n’zothandiza kwambiri ku mpingo wanu, kuti zikambidwe mlungu wina m’mwezi womwewo.