Ndandanda ya Mlungu wa April 6
MLUNGU WOYAMBIRA APRIL 6
Nyimbo Na. 51 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 11 ndime 1-8 ndi chigawo chachiwiri patsamba 107 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Samueli 16-18 (Mph. 8)
Na. 1: 1 Samueli 18:17-24 (Osapitirira mph. 3)
Na. 2: Kodi Mulungu Ndi Amene Amachititsa Kuti Anthu Azivutika?—igw tsa. 14 ndime 1-4 (Mph. 5)
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kupewa Kudzikuza?—bt tsa. 81-82 ndime 17-21 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: ‘Khalani Okonzekera Ntchito Iliyonse Yabwino.’—Tito 3:1.
Mph. 10: Zimene Munganene Pogawira Magazini a April. Nkhani yokambirana. Yambani ndi kuchita chitsanzo cha mmene tingagawirire magaziniwo pogwiritsa ntchito zitsanzo za ulaliki zimene zili patsamba lino. Kenako kambiranani zitsanzo za ulalikizo kuyambira poyamba mpaka pamapeto.
Mph. 10: Kodi Tinachita Zotani? Nkhani yokambirana. Pemphani omvera kuti afotokoze mmene anapindulira pogwiritsa ntchito malangizo a m’nkhani yakuti, “Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Pezani Anthu Oti Muziwapatsa Magazini Mwezi Uliwonse.” Pemphani omvera kuti afotokoze zinthu zosangalatsa zomwe anakumana nazo.
Mph. 10: Zofunika pampingo.
Nyimbo Na. 106 ndi Pemphero