Ndandanda ya Mlungu wa April 20
MLUNGU WOYAMBIRA APRIL 20
Nyimbo Na. 112 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 11 ndime 17-22 ndi bokosi patsamba 116 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Samueli 23-25 (Mph. 8)
Na. 1: 1 Samueli 23:13-23 (Osapitirira mph. 3)
Na. 2: Kodi Baibulo Limalonjeza Chiyani Zam’tsogolo?—igw tsa. 16 ndime 1-3 (Mph. 5)
Na. 3: Pewani Kudzikonda Potumikira Yehova—Yer. 45:2-5 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: “Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.”—Aef. 5:15, 16.
Mph. 15: “Tingalalikire Bwanji Pogwiritsa Ntchito Tebulo Kapena Kashelefu Kamatayala?” Nkhani yokambirana. Chitani chitsanzo ichi: Ofalitsa awiri akulalikira pogwiritsa ntchito tebulo kapena kashelefu kamatayala. Pakudutsa munthu ndipo wofalitsa wina akumumwetulira. Kenako pakudutsanso munthu wina, wofalitsa winayo akumumwetulira ndipo munthuyo akufika pafupi. Kenako wofalitsayo akuyamba kuyankhula naye. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji zomwe taphunzira m’chitsanzochi ngakhale titakhala kuti sitikulalikira pogwiritsa ntchito tebulo kapena kashelefu kamatayala?
Mph. 15: Misonkhano Yachigawo Imakhala Nthawi Yosangalatsa. Nkhani yokambirana yochokera mu Nsanja ya Olonda ya September 15, 2012, tsamba 31-32 ndime 15-19. Limbikitsani omvera kuti asadzalephere kupita kumsonkhano wachigawo womwe ukubwerawu. Alimbikitseninso kuti aone pulogalamu yomwe ili pa webusaiti yathu ya jw.org/ny n’cholinga choti adziwiretu nkhani zolimbikitsa zomwe zidzakambidwe ku msonkhanoko.
Nyimbo Na. 75 ndi Pemphero