Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu June: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? kapepala kakuti, Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? komanso timapepala tomwe tatuluka posachedwapa. July ndi August: Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu kapena Mverani Mulungu ndi kakuti, Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha. September ndi October: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!
◼ Muzilemba chiwerengero cha timapepala tonse timene mwagawira kuphatikizapo timapepala toitanira anthu kumsonkhano kapena timene mwasiya pa nyumba imene simunapezepo anthu pa danga lakuti “Timabuku” mukamapereka lipoti lanu la utumiki wakumunda kumapeto kwa mwezi. Ngati munthu wasonyeza chidwi ndipo walandira mabuku athu, ngakhale kapepala, muziyesetsa kuchita ulendo wobwereza kuti apitirize kukhala ndi mtima wofuna kuphunzira Mawu a Mulungu.
◼ Kumbukirani kuti simuyenera kuchita misonkhano ya mpingo mkati mwa mlungu umene mukuyembekezera kupita kumsonkhano wachigawo. Zimenezi zimapereka mwayi kwa abale woti akonzekere msonkhanowo. Patapita mwezi umodzi kapena iwiri msonkhanowu utachitika, konzani zoti mudzakambirane mfundo zomwe ofalitsa aona kuti n’zothandiza pamene akugwira ntchito yolalikira. Mungachite zimenezi pa nthawi ya zofunika pampingo.