Ndandanda ya Mlungu wa July 6
MLUNGU WOYAMBIRA JULY 6
Nyimbo Na. 79 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 15 ndime 11-19 (30 min.)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Mafumu 7-8 (8 min.)
Na. 1: 1 Mafumu 8:27-34 (Osapitirira 3 min.)
Na. 2: Yehova Alibe Tsankho—bt tsa. 71-72 ndime 11-14 (5 min.)
Na. 3: Kodi Mungatani Kuti Musamade Nkhawa?—igw tsa. 24 1-3 (5 min.)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: “Kumbukirani masiku akale”—Deut. 32:7.
10 min: Zimene Munganene Pogawira Magazini mu July. Nkhani yokambirana. Yambani ndi kuchita chitsanzo chosonyeza zimene tinganene pogawira magaziniwa pogwiritsa ntchito zitsanzo zaulaliki zomwe zili patsamba lino. Kenako kambiranani chitsanzo cha ulaliki chilichonse kuyambira poyambirira mpaka pamapeto.
10 min: “Ntchito Yoitanira Anthu ku Msonkhano Wachigawo.” Mafunso ndi mayankho. Mukamaliza kukambirana ndime yachitatu, chitani chitsanzo chachidule chosonyeza mmene mungagawirire kapepalaka.
10 min: Zofunika Kukumbukira pa Msonkhano Wachigawo wa 2015. Nkhani yokambidwa ndi mlembi. Thandizani omvera kuti amvetse mfundo zopezeka m’malemba omwe ali m’nkhaniyi. Athandizeninso kuona mmene angagwiritsire ntchito mfundo zake pa nthawi ya msonkhano wachigawo wa 2015. Kambirananinso mfundo zokhudza kupewa ngozi pamisonkhano yathu, zimene mukuona kuti n’zothandiza, zomwe zikupezeka m’kalata ya deti la August 3, 2013, yopita ku mipingo yonse.
Nyimbo Na. 67 ndi Pemphero