Ndandanda ya Mlungu wa July 27
MLUNGU WOYAMBIRA JULY 27
Nyimbo Na. 50 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 16 ndime 10-17 (30 min.)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Kuwerenga Baibulo: 1 Mafumu 15-17 (8 min.)
Na. 1: 1 Mafumu 15:16-24 (Osapitirira 3 min.)
Na. 2: Kodi Baibulo Lingathandize Bwanji Akazi?—igw tsa. 26 ndime 3-4 (5 min.)
Na. 3: Kodi Achinyamata Angakonzekere Bwanji Kutumikira Yehova Molimba Mtima?—dp tsa. 36-38 ndime 15-19 (5 min.)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: ‘Pitani mukaphunzitse anthu kuti akhale ophunzira anga.’—Mat. 28:19, 20.
10 min: Kodi Mukuwonjezera Luso Lanu mu Utumiki? Nkhani yokambirana. Fotokozani mfundo zomwe zili m’ndime yoyamba ya nkhani yakuti, “Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki,” yomwe ili mu Utumiki wa Ufumu wa February 2014. Ndimeyi inafotokoza cholinga cha nkhani zakuti, “Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki.” Tchulani mwachidule mfundo zomwe zinali m’nkhani zina za mutu umenewu, zomwe zinatuluka mu Utumiki wa Ufumu. Pemphani omvera kuti afotokoze mmene apindulira ndi nkhanizi. Limbikitsani omvera kuti azitsatira malangizo a nkhanizi pochita zomwe zimapezeka pakamutu kakuti, “Tayesani Kuchita Izi Mwezi Uno.”
10 min: Muzigwiritsa Ntchito Kabuku Kakuti, Kodi M’Baibulo Muli Nkhani Zotani? Pothandiza Munthu Amene Mumaphunzira Naye. Nkhani yokambirana. Kambiranani mmene tingagwiritsire ntchito mbali zotsatirazi, zomwe zili m’kabukuka, pothandiza munthu amene timaphunzira naye kuti azipindula kwambiri ndi Baibulo. (1) “Kodi Mungapeze Bwanji Malemba a M’Baibulo?” (2) Funso 19: “Kodi m’mabuku a m’Baibulo muli zotani?” (3) Funso 20: ”Kodi mungatani kuti muzipindula kwambiri mukamawerenga Baibulo?” Pomaliza chitani chitsanzo chosonyeza wofalitsa akukambirana imodzi mwa mbali zimenezi ndi munthu amene amaphunzira naye Baibulo, atamaliza phunziro.
10 min: “Zinthu Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa.” Mafunso ndi mayankho.
Nyimbo Na. 125 ndi Pemphero