Ndandanda ya Mlungu wa September 7
MLUNGU WOYAMBIRA SEPTEMBER 7
Nyimbo Na. 113 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 18 ndime 9-19 (30 min.)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 2 Mafumu 12-15 (8 min.)
Na. 1: 2 Mafumu 13:12-19 (Osapitirira 3 min.)
Na. 2: Akhristu Enieni Amachita Ntchito Zambiri Zabwino—bt tsa. 67 (5 min.)
Na. 3: Kodi M’Malemba Achigiriki Muli Zotani?—igw tsa. 31 (5 min.)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: “Ine ndi a m’nyumba yanga, tizitumikira Yehova.”—Yos. 24:15.
10 min: Kodi Tinachita Zotani? Nkhani yokambirana. Pemphani omvera kuti afotokoze mmene anapindulira pogwiritsa ntchito malangizo a m’nkhani yakuti, “Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Muziphunzitsa Ofalitsa Atsopano.” Kenako apempheni kuti anene zinthu zosangalatsa zimene anakumana nazo.
10 min: Kodi Banja Lanu Limafika Pamisonkhano Nthawi Zonse? Nkhani yochokera palemba la Aheberi 10:24, 25. Funsani banja lomwe lili ndi ana. Kodi bambo wa m’banjalo amatani kuti aliyense m’banja lake aziona kuti misonkhano ndi yofunika kwambiri? Kodi aliyense m’banjamo amayenera kuchita chiyani kuti banja lawo lizipezeka pamisonkhano nthawi zonse? Nanga amatani kuti zimenezi zitheke? Kodi banjalo limakonzekera liti misonkhano? Pomaliza, limbikitsani omvera kuti azipezeka pamisonkhano nthawi zonse komanso aziyankhapo.
10 min: Kodi Mungafese Mbewu za Choonadi mwa Kulalikira Achibale Anu? (Mac. 10:24, 33, 48) Nkhani yochokera mu Buku Lapachaka la 2015, tsamba 87 ndime 1-2 ndi tsamba 90 ndime 1-3. Pemphani omvera kuti afotokoze zimene tikuphunzirapo.
Nyimbo Na. 118 ndi Pemphero