Ndandanda ya Mlungu wa November 9
MLUNGU WOYAMBIRA NOVEMBER 9
Nyimbo Na. 44 ndi Pemphero
cl mutu 21 ndime 9-15 (30 min.)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Mbiri 21-25 (8 min.)
Na. 1: 1 Mbiri 23:1-11 (Osapitirira 3 min.)
Na. 2: Kodi Munthu Ali ndi Mzimu Umene Suufa?—bh tsa. 209-211 (5 min.)
Na. 3: Kodi Aramagedo N’chiyani?—rs tsa. 37-38 ndime 5 (5 min.)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezu Uno: “Ineyo ndinabzala, Apolo anathirira, koma Mulungu ndiye anakulitsa.”—1 Akor. 3:6.
10 min: “Ineyo Ndinabzala, Apolo Anathirira, Koma Mulungu Ndiye Anakulitsa.” Nkhani yochokera pa mutu wa mwezi uno. (1 Akor. 3:6) Ngati nthawi ilipo, fotokozani mfundo za mu Nsanja ya Olonda ya March 1, 1993, tsamba 20 mpaka 23. Fotokozani mwachidule nkhani zimene tiphunzire pa Msonkhano wa Utumiki mwezi wa November ndiponso kugwirizana kwake ndi mutu wa mweziwu.
20 min: “Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Kugawira Buku Lakuti Baibulo Limaphunzitsa Chiyani.” Nkhani yokambirana. Chitani zitsanzo ziwiri. Chitsanzo chimodzi chisonyeze zimene zafotokozedwa mu nkhaniyi, china chisonyeze njira imene mukuona kuti imathandiza kwambiri.
Nyimbo Na. 111 ndi Pemphero