Ndandanda ya Mlungu wa November 16
MLUNGU WOYAMBIRA NOVEMBER 16
Nyimbo Na. 65 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 21 ndime 16-21 ndi bokosi patsamba 217 (30 min.)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Mbiri 26-29 (8 min.)
Na. 1: 1 Mbiri 29:20-30 (Osapitirira 3 min.)
Na. 2: Ziwanda Sizingalepheretse Ntchito Yophunzitsa Mawu a Mulungu—bt tsa. 161-163 ndime 13-15 (5 min.)
Na. 3: Kodi Mumalemekeza Chikumbumtima cha Anzanu?—lv tsa. 19-21 ndime 12-15 (5 min.)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezu Uno: “Ineyo ndinabzala, Apolo anathirira, koma Mulungu ndiye anakulitsa.””—1 Akor. 3:6.
10 min: Pitirizani ‘Kuthirira’ Anthu Amene Asonyeza Chidwi. (1 Akor. 3:6-8) Funsani mpainiya wokhazikika komanso wofalitsa. Kodi iwo amatani kuti akhale ndi maulendo obwereza? Kodi amakonzekera bwanji? Kodi amatani kuti apezenso munthu kunyumba kwake? Nanga ndi zinthu ziti zosangalatsa zimene zinachitika chifukwa chochita ulendo wobwereza?
20 min: “Kodi Tingagwiritse Ntchito Bwanji Zinthu Zimene Zinajambulidwa Kuti Tizimvetsera?” Mafunso ndi mayankho. Limbikitsani anthu amene ali ndi mwayi wogwiritsa ntchito Intaneti kuti azimvetsera zinthuzi paokha komanso azizigwiritsa ntchito mu utumiki.
Nyimbo Na. 108 ndi Pemphero