Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb16 April tsamba 4
  • April 11-17

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • April 11-17
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
mwb16 April tsamba 4

April 11-17

YOBU 21-27

  • Nyimbo Na. 83

  • Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

  • “Yobu Sanalole Kuti Maganizo Olakwika Amusokoneze”: (10 min.)

    • Yobu 22:2-7—Elifazi anapatsa Yobu malangizo popanda umboni woti analidi wolakwa (w06 3/15 15 ndime 6; w05 9/15 26-27; w95 2/15 27 ndime 6))

    • Yobu 25:4, 5—Bilidadi anauza Yobu maganizo olakwika (w05 9/15 26-27)

    • Yobu 27:5, 6—Yobu sanalole kuti zonena za ena zimuchititse kudziona ngati walephera kukhala ndi mtima wosagawanika (w09 8/15 4 ndime 8; w06 3/15 15 ndime 8)

  • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

    • Yobu 24:2—Kodi n’chifukwa chiyani munthu yemwe wasuntha malire a mnzake ankaonedwa kuti wapalamula mlandu waukulu? (it-1-E 360)

    • Yobu 26:7—Kodi ndi mfundo iti yochititsa chidwi imene Yobu ananena yokhudza mmene dziko liliri? (w15 6/1 5 ndime 4; w11 7/1 26 ndime 2-5)

    • Kodi ndaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

    • Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?

  • Kuwerenga Baibulo: Yobu 27:1-23 (Osapitirira 4 min.)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

  • Ulendo Woyamba: g16.2 Tsamba loyamba-Muuzeni nkhani imene mudzakambirane ulendo wotsatira. (Osapitirira 2 min.)

  • Ulendo Wobwereza: g16.2 Tsamba loyamba-Muuzeni nkhani imene mudzaphunzire ulendo wotsatira. (Osapitirira 4 min.)

  • Phunziro la Baibulo: bh tsa. 145 ndime 3-4 (Osapitirira 6 min.)

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

  • Nyimbo Na. 129

  • Kodi Mungatani Kuti Anzanu Asiye Kukuvutitsani?: (15 min.) Nkhani yokambirana. Yambani ndi kuonetsa vidiyo ya pawebusaiti yathu ya jw.org/ny yakuti, Kodi Mungatani Kuti Anzanu Asiye Kukuvutitsani? (Pitani pamene palembedwa kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ACHINYAMATA.) Kenako kambiranani mafunso otsatirawa: Kodi munthu angavutitsidwe pazifukwa ziti? Kodi munthu yemwe amavutitsidwa angakumane ndi mavuto ati? Kodi mungatani ngati anzanu amakuvutitsani kapenanso kuti asamakuvutitseni? Kodi mungauze ndani ngati wina akukuvutitsani? Pomaliza fotokozani mfundo za m’buku la Mayankho a Zimene Achinyamata Amadzifunsa, Buku Lachiwiri mutu 14.

  • Phunziro la Baibulo la Mpingo: cl mutu 28 ndime 18-21 ndi bokosi patsamba 289 (30 min.)

  • Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)

  • Nyimbo Na. 23 ndi Pemphero

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena