CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YEREMIYA 12-16
Aisiraeli Anaiwala Yehova
Yeremiya anapatsidwa ntchito yovuta kwambiri imene inasonyeza zimene Yehova ankafuna kuchita powononga Aisiraeli osamva a ku Yuda ndiponso ku Yerusalemu.
Yeremiya anagula lamba wansalu
Anamanga lambayo m’chiuno ndipo zinkaimira ubwenzi wolimba umene Aisiraeli akanakhala nawo ndi Yehova
Yeremiya anatenga lambayo n’kupita naye kumtsinje wa Firate
Iye anamubisa mumng’alu wa m’phanga n’kubwerera ku Yerusalemu
Yeremiya anabwereranso kumtsinje wa Firate kukatenga lambayo
Anali atawonongeka
Yehova anafotokoza tanthauzo la zimenezi pambuyo poti Yeremiya wamaliza ntchitoyi
Ntchitoyi inkaoneka ngati yopanda pake, komabe Yeremiya anamvera ndi mtima wonse ndipo izi zinathandiza kuti Yehova afike anthuwo pamtima