May 22-28
YEREMIYA 44-48
Nyimbo Na. 70 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Leka ‘Kufunafuna Zinthu Zazikulu’”: (10 min.)
Yer. 45:2,3—Baruki sankasangalala chifukwa cha maganizo olakwika amene anali nawo (jr 104-105 ¶4-6)
Yer. 45:4,5a—Yehova anathandiza Baruki mokoma mtima (jr 103 ¶2)
Yer. 45:5b—Baruki anapulumutsa moyo wake chifukwa choika maganizo ake pa zinthu zofunika kwambiri (w16.07 8 ¶6)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Yer. 48:13—N’chifukwa chiyani ‘Amowabu anachita manyazi ndi Kemosi’? (it-1-E 430)
Yer. 48:42—Kodi kuganizira za chiweruzo chimene Yehova anapereka kwa Amowabu kungalimbitse bwanji chikhulupiriro chathu? (it-2-E 422 ¶2)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Yer. 47:1-7
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) hf—Muuzeni nkhani imene mudzakambirane ulendo wotsatira.
Ulendo Wobwereza: (Osapitirira 4 min.) hf—Muuzeni nkhani imene mudzakambirane ulendo wotsatira.
Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) lv 199 ¶9-10—Mwachidule sonyezani wophunzira mmene angafufuzire malangizo pa nkhani yokhudza vuto linalake limene akukumana nalo.
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Achinyamata—Musamafunefune Zinthu Zazikulu: (15 min.) Onetsani ndiponso kukambirana vidiyo yakuti Zimene Achinyamata Amafunsa—Kodi Ndidzachita Zotani Pamoyo Wanga?—Zimene Anasankha.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) kr mutu 1 ¶1-10 komanso Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 17 ndi Pemphero