June 19-25
EZEKIELI 1-5
Nyimbo Na. 75 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Ezekieli Ankasangalala Kulengeza Uthenga wa Mulungu”: (10 min.)
[Onetsani vidiyo yakuti, Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Ezekieli.]
Ezek. 2:9–3:2—Ezekieli anadya mpukutu wokhala ndi “nyimbo zoimba polira, mawu odandaula ndi mawu olira” (w08 7/15 8 ¶6-7; it-1-E 1214)
Ezek. 3:3—Ezekieli ankasangalala kutumikira Yehova monga mneneri (w07 7/1 12 ¶3)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Ezek. 1:20, 21, 26-28—Kodi galeta lakumwamba limaimira chiyani? (w07 7/1 11 ¶6)
Ezek. 4:1-7—Kodi Ezekieli anachitadi zinthu zofanizira kuzingidwa kwa Yerusalemu? (w07 7/1 12 ¶4)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Ezek. 1:1-14
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) T-32—Muuzeni zimene mudzakambirane ulendo wotsatira.
Ulendo Wobwereza: (Osapitirira 4 min.) T-32—Muonetseni Vidiyo Yothandiza Pogawira Kabuku Kakuti Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala, kenako mugawireni kabukuko.
Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) bh 143 ¶20-21—Sonyezani mmene tingafikire pamtima wophunzira wathu.
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Muzisangalala Mukamalalikira Uthenga Wabwino”: (15 min.) Nkhani yokambirana. Onetsani vidiyo yakuti Kusinkhasinkha Kungatithandize Kukhala Wosangalala (imapezeka pamene palembedwa kuti BAIBULO).
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) kr mutu 2 ¶23-34
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 32 ndi Pemphero