Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya August 2017
AUGUST 7-13
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EZEKIELI 28-31
it-2 1136 ¶4
Turo
Kuwonongedwa kwa Mzindawu. Nebukadinezara anazinga mzinda wa Turo kwa nthawi yayitali, ndipo mutu wa msilikali wake aliyense “unameteka” chifukwa cha kutentha kwa zipewa zawo ndipo mapewa awo “ananyuka” chifukwa chonyamula katundu amene ankagwiritsa ntchito. Popeza kuti Nebukadinezara sanalandire “malipiro” aliwonse pa ntchito yovuta imene anagwira yogonjetsa Turo, Yehova analonjeza kuti adzamupatsa chuma cha ku Iguputo. (Ezek. 29:17-20) Malinga ndi zimene wolemba mbiri wina wachiyuda dzina lake Josephus analemba, asilikali a Babulo anazinga mzindawo kwa zaka 13 (Against Apion, I, 156 [21]), ndipo zimenezi sizinali zophweka. Olemba mbiri samafotokoza zonse zimene Nebukadinezara anachita polanda mzindawo. Koma zikuoneka kuti katundu wambiri wa ku Turo anawonongeka ndipo anthu ambiri anaphedwa.—Ezek. 26:7-12.
it-1 698 ¶5
Iguputo, Aiguputo
Zolemba zina za ku Babulo zomwe zapezeka, zimene zinalembedwa m’chaka cha 37 (588 B.C.E.) cha ulamuliro wa Nebukadinezara, zimafotokoza kuti Ababulo ankafuna kuukira Iguputo. Popeza kuti zina sizinapezekebe, sizikudziwika ngati zolembazo zimafotokoza zimene asilikali a Ababulowo ankachita pa nthawi yokagonjetsa dziko la Iguputolo. Komabe Nebukadinezara ndi asilikali ake analanda chuma cha Iguputo kuti chikhale malipiro pa ntchito imene anagwira yopereka chiweruzo cha Yehova kwa anthu a ku Turo, omwe ankatsutsa atumiki a Mulungu.—Ezek. 29:18-20; 30:10-12.
g86 11/8 27 ¶4-5
Kodi Tiyenera Kupereka Misonkho Yonse?
Kuti tiyankhe funsoli, tiyenera kuganizira zimene Mulungu anachita polipira boma lina limene linagwira ntchito imene iyeyo ankafuna. Pofuna kuchita zinthu mwachilungamo, Yehova analamula kuti mzinda wa Turo uwonongedwe. Iye anagwiritsa ntchito Nebukadinezara ndi asilikali ake kuti akawononge mzindawo ndipo zimenezi sizinali zophweka ngakhale kuti Ababulowo anali amphamvu. Choncho Yehova anaona kuti iwo ayenera kulandira malipiro. Lemba la Ezekieli 29:18, 19 limati: “Iwe mwana wa munthu, Nebukadirezara mfumu ya Babulo anatuma gulu lake lankhondo kukachita utumiki wofunika kwambiri pomenyana ndi Turo. . . . Koma mfumuyo ndi gulu lake lankhondo sanalandire cholowa chilichonse pa utumiki umene anachita pomenyana ndi Turo. Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ine ndipereka dziko la Iguputo kwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo. Adzatenga chuma chake chochuluka ndi kulanda zinthu zake zambiri. Zimenezi zidzakhala malipiro a gulu lake lankhondo.’”
Ophunzira Baibulo ankadziwa kuti Nebukadinezara anali wodzikuza, womva zake zokha komanso sankalambira Mulungu. Asilikali komanso anthu a ku Babulo ankakonda kuchitira nkhanza anthu omwe awagwira ukapolo. Ngakhale kuti Yehova sankasangalala ndi zimenezi, anaona kuti ayenera kuwapatsabe malipiro onse amene anawalonjeza.
it-2 604 ¶4-5
Ungwiro
Woyamba kukhala wochimwa komanso mfumu ya Turo. Zimene timawerenga pa Genesis 3 komanso mawu a Yesu omwe ali pa Yohane 8:44, zimasonyeza kuti cholengedwa chauzimu ndi chimene chinayamba kuchimwa kenako n’kuchititsanso kuti anthu achimwe. Nyimbo yolira ya pa Ezekieli 28:12-19 yomwe imanena za “mfumu ya Turo,” imafotokoza zofanana ndi zimene Satana anachita polephera kumvera Mulungu. “Mfumu ya Turo” inali yonyada, inadzipanga kukhala mulungu, komanso ikutchedwa “kerubi” yemwe anali mu “Edeni, munda wa Mulungu.” Zimenezi sizikusiyana ndi zochita za Satana Mdyerekezi yemwe ndi wonyada komanso amadziwika monga njoka ya mu Edeni. Satana amatchedwanso “mulungu wa nthawi ino.”—1 Tim. 3:6; Gen. 3:1-5, 14, 15; Chiv. 12:9; 2 Akor. 4:4.
Mfumu ya Turo imeneyi siimadziwika, koma inkadziona kuti ndi “chiphadzuwa,” inali ndi ‘nzeru zochuluka ndiponso yokongola kwambiri,’ komanso ‘yopanda cholakwa [kuchokera ku liwu lachiheberi ta·mimʹ]’ kuyambira nthawi imene inalengedwa kufikira pamene inachita zinthu zosalungama. (Ezek. 27:3; 28:12, 15) Zimene zinalembedwa mu nyimbo ya m’buku la Ezekieli ziyenera kuti zimanena za mafumu onse a ku Turo osati mfumu imodzi yokha. (Yerekezerani ndi ulosi wonena za mfumu ya Babulo wa pa Yes. 14:4-20.) Kumayambiriro mafumu a Turo ankagwirizana ndi anthu a Mulungu, moti pa nthawi ya ulamuliro wa Mfumu Davide komanso Solomo, iwo anapereka zinthu zoti zithandize pomanga kachisi wa Yehova kuphiri la Moriya. Apa tingati mafumu a Turo analibe cholakwa chifukwa ankakomera mtima Aisiraeli omwe anali anthu a Yehova. (1 Maf. 5:1-18; 9:10, 11, 14; 2 Mbiri 2:3-16) Koma mafumu amene anabwera pambuyo pake, anachita zosiyana ndi mafumu oyambawo ndipo Mulungu anawadzudzula pogwiritsa ntchito aneneri ake monga Yoweli, Amosi komanso Ezekieli. (Yow. 3:4-8; Amosi 1:9, 10) Kuwonjezera pa kufotokoza kufanana kwa “mfumu ya Turo” ndi mdani wamkulu wa Mulungu, ulosiwu umasonyezanso kuti palibe munthu amene angachite zinthu ‘mwangwiro’ komanso popanda ‘kulakwitsa’ kalikonse.
AUGUST 14-20
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EZEKIELI 32-34
it-2 1172 ¶2
Mlonda
Zimene Amaimira. Yehova anaika aneneri omwe ankatumikira ngati alonda ophiphiritsira a Aisiraeli (Yer. 6:17) ndipo iwonso nthawi zina ankatchula za alonda ophiphiritsira. (Yes. 21:6, 8; 52:8; 62:6; Hos. 9:8) Aneneri omwe anali ngati alondawa anali ndi udindo wochenjeza anthu oipa kuti awonongedwa, ndipo akapanda kutero, ankakhala ndi mlandu. Koma akapereka chenjezo, anthu n’kulephera kumvera, mlandu wa magazi unkakhala pa anthu osamverawo. (Ezek. 3:17-21; 33:1-9) Mneneri wosakhulupirika anali wopanda phindu mofanana ndi mlonda wakhungu kapena galu wosauwa.—Yes. 56:10.
Pitirizani Kulalikira za Ufumu
Kupewa Mlandu wa Magazi
Mofanana ndi Ezekieli, a Mboni za Yehova ali ndi udindo wochenjeza anthu za chiweruzo cha Mulungu chomwe chikubwera. Ezekieli anaikidwa kuti akhale mlonda wa nyumba ya Isiraeli. Ntchito yake inali yoti achenjeze Aisiraeli kuti awonongedwa ngati sasiya kuchita zoipa. Ngati iye akanalephera kupereka chenjezoli, anthu oipawo akanawonongedwabe, koma mlandu wamagazi ukanakhala pamutu pake. Yehova anasonyeza mmene amaonera nkhani yopereka chiweruzo, iye anati: “Ine sindisangalala ndi imfa ya munthu woipa, koma ndimafuna kuti munthu woipa abwerere kusiya njira zake n’kukhala ndi moyo. Bwererani! Bwererani ndi kusiya njira zanu zoipa. Muferenji inu a nyumba ya Isiraeli?”—Ezekieli 33:1-11.
AUGUST 21-27
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EZEKIELI 35-38
Kufufuza Mfundo Zothandiza
“Adzadziwa Kuti Ine Ndine Yehova”
Ayuda otsala atabwerera kwawo, dziko lawo lomwe linali bwinja linasintha n’kukhala lobala zipatso ngati “munda wa Edeni.” (Werengani Ezekieli 36:33-36.) Mofanana ndi zimenezi, kuyambira mu 1919 Yehova anachititsa kuti odzozedwa amene adakali padzikoli akhale m’paradaiso wauzimu wobala zipatso ndipo a “khamu lalikulu” nawonso akusangalala nawo limodzi. Popeza kuti m’paradaisoyu muli anthu oyera, Mkhristu aliyense amene anadzipereka kwa Yehova ayenera kuyesetsa kukhala woyera.—Ezekieli. 36:37, 38.
AUGUST 28–SEPTEMBER 3
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EZEKIELI 39-41
Kufufuza Mfundo Zothandiza
Kutsegula Njira Yobwerera ku Paradaiso
Kodi zida zankhondo zimene mitundu ya anthu idzasiye zidzagwiritsidwa ntchito yotani? Ezekieli anatchula mophiphiritsira kutalika kwa nthawi yowonongera zida zankhondo, ndipo izi zikusonyeza kuti zidazi ndi zambiri. (Ezekieli 39:8-10) N’kutheka kuti anthu amene adzapulumuke pa Aramagedo adzagwiritsa ntchito mbali zina zotsala za zidazi pa ntchito zosiyanasiyana zothandiza.—Yesaya 2:2-4.