September 18-24
Danieli 1-3
Nyimbo Na. 131 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Kukhala Okhulupirika kwa Yehova Kumabweretsa Madalitso”: (10 min.)
[Onetsani vidiyo yakuti Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Danieli.]
Dan. 3:16-20—Anzake a Danieli analimba mtima n’kukana kuchita zinthu zimene zikanawapangitsa kuti akhale osakhulupirika kwa Yehova (w15 7/15 25 ¶15-16)
Dan. 3:26-29—Kukhulupirika kwawo kunachititsa kuti Yehova atamandidwe ndipo anawadalitsa (w13 1/15 10 ¶13)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Dan. 1:5, 8—N’chifukwa chiyani Danieli ndi anzake atatu aja ankaona kuti adetsedwa akadya zakudya zabwino zochokera kwa mfumu? (it-2 382)
Dan. 2:44—N’chifukwa chiyani Ufumu wa Mulungu udzaphwanye maufumu a padziko lapansi omwe ndi mbali zosiyanasiyana za chifaniziro chomwe Nebukadinezara analota? (w12 6/15 17, bokosi; w01 10/15 6 ¶4)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Dan. 2:31-43
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Yes. 40:22—Kuphunzitsa Choonadi—Muuzeni zimene mudzakambirane ulendo wotsatira.
Ulendo Wobwereza: (Osapitirira 4 min.) Aroma 15:4—Kuphunzitsa Choonadi—Musiyireni khadi lodziwitsa anthu za JW.ORG.
Nkhani: (Osapitirira 6 min.) w17.02 29-30—Mutu: Kodi Yehova Amayamba Waganizira Kaye Zimene Tingapirire Ndiyeno N’kusankha Mayesero Oti Tikumane Nawo?
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Muzikhala Okhulupirika Mukakumana ndi Mayesero”: (8 min.) Nkhani yokambirana.
“Muzikhala Okhulupirika Wachibale Wanu Akachotsedwa”: (7 min.) Nkhani yokambirana.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) kr mutu 7 ¶1-9
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 101 ndi Pemphero